KWATHA! CHAKWERA WATHETSA MILANDU YA CHIZUMA

President Lazarus Chakwera walamula kuti milandu yonse yomwe mkulu wa bungwe la ACB, Martha Chizuma akuzengedwa ithe.
Mkulu ozenga milandu ya boma, Masauko Chamkakala watsimikiza izi ndipo wati walankhula kale ndi magulu onse okhudzidwa kuphatikizapo ofesi ya mlangizi wa boma paza malamulo.
A Chizuma amayankha mulandu olingana ndi zomwe adalankhulana ndi a Anderson Mwakyeru pa lamya zokhudza ofesi yawo.
Izi zikudza patapita masiku ochepa boma litapeza maloya awiri apadera kuti athandizire pa nkhani-yi maka kutsutsa ganizo loti a Chizuma asaime pa ntchito.
Dziko la America lidanenetsa kuti boma la Malawi likapitilira kuzunza a Chizuma lipereka zilango zina kudziko lino ponena kuti utsogoleri wa dziko sukuwonetsa chidwi cholimbana ndi katangale.