Adindo ayamikira DC wa ku Nsanje

Anthu osiyana siyana m’boma la Nsanje ayamikira bwana mkubwa wa bomali, Dr Medson Matchaya kamba kachidwi chake pa nkhani zachitukuko zosiyana siyana.
Phungu wa ku nyumba ya malamul wa chigawo cha pakati mb’oma la Nsanje, Kafandikhale Mandevana wati chibwelereni bwanam’kubwayi, zitukuko zambiri zikumalizika bwinobwino pamene mmbuyomu zitukuko zambiri zimayimira panjira zomwe akuti zimawabwezeletsa mmbuyo.
Mandevana amalankhula izi pamene wachiwiri kwa nduna yamaboma ang’ono Halima Daudi anakayendera zitukuko zosiyanaziyana m’bomali.
Poyankhulaponso pa mwambo womwewo wapampando wa khonsolo ya Nsanje, Rose Makiyi anati ndiokhutira kwambiri ndi chidwi chomwe bwanam’kubwa wawo ali nacho pankhani zachitukuko.Iwo anati zitukuko zambiri m’bomali zinkaimira panjira kamba koti mmbuyomo ma contractor amapatsidwa ndalama zitukuko zisanathe zomwe zimapangitsa ma contractor kusiyira ntchito panjira ndikuthawa.
Makiyi anati: “chibwelereni bwanam’kubwayu anatilimbikitsa akuluakulu ku nkhonsoloyi kuti tidzitsatira ndondomeko zoyenera ndikusiya kupeleka ndalama kwa ma contractor ntchito isananthe.”
Mawu ake mfumu yaikulu chimombo anathokoza nduna ya maboma ang’ono kamba kotumiza Matchaya ku Nsanje ponena kuti kubwela kwawo kwapangitsa zinthu zambiri kuti zisithe, Chimombo anati boma la Nsanje linari ndi mavuto ochuluka pa nkhani yazituko zomwe akuti zimapangisa bomali kuti isapite pasogolo pa chuma.
Mmawu ake mkulu wa zitukuko za Governance enabled Service Delivery, (GESD) a Charles Chunga adati ndiwonkhutira ndi mmene khonsolo ya Nsanje yayendetsera zitukuko za Thumba la GESD.
Chiwunga anati: “Khonsoloyi inasankha ma pulojekiti omwe anthu amawafuna zomwe akuti nzonyadilitsa.A Chiwunga ati ntchito zomanga manga zomwe nkhonsoyi yamanga kudzera mu thumba la ndalama kuchokera kuchokera ku bank yayikulu padziko lonse la Word Bank akuti zamangidwa molimba kwambiri polingalira kuti boma la nsanje limankhudzidwa kwambiri ndi madzi osefukirawo anati bungwe lawo ndilokhutira kwambiri ndi momwe bomali lagwilira ntchito zake ponena kuti ma pulojekiti onse omwe amangidwa mb’omali anaika zonse zofunikira mchimake monga zimbudzi mwazina.